Charles Kachitseko wazaka 33, yemwe wakhala akusowa atadumphila mnyanja ya Malawi kuchokera mu sitima ya MV Ilala lachiwiri usiku wapezeka atafa m'boma la Nkhotakota.
Malinga ndi womwe awona izi asodzi ndi amene apeza thupi la mzibamboyo likuyandama.
Pakadali pano zotsatila zakupima kwa thupilo pa chipatala cha Nkhotakota zikusonyeza kuti Kachitseko wafa kamba kakubanika.
Achibale pamodzi ndi anthu ena ayika kale m'manda thupilo pafupi ndi Dooko la Kaliba m'boma lomwelo.
Kachitseko amachokera m'mudzi wa Mwansambo TA Mwansambo ku Nkhotakota komweko ndipo anthu amene anamuwona asanadumphe kuchokera mu sitimayo akuti mkuluyo amamwa mowa mu sitima yomweyo.
(Daire Media Group)

Comments
Post a Comment