Aku likulu la Police mdziko muno ati akusakasaka wa police amene akumuganizira kuti wapha bwenzi lake ku Zomba.
Mneneri ku likulu la Polisi Peter kalaya wati Sergeant Peter Chimoyo, anayamba wamenya bwenzi lawolo atasemphana maganizo.
Mayiyo anapita ku chipatala cha Domasi kumene wakamwalilira akulandila thandizo la mankhwala.
Malimga ndi Kalaya mulandu womwe wapalamula Chimoyo chilango chake ndikukhala ku Ndende moyo wake wonse.
Daire Media Group

Comments
Post a Comment