Nduna yakale yazachuma Joseph Mwanamveka ayimanga pamodzi ndi anthu ena anayi powaganizira kuti akukhudziwa pa milanudu yokhuza katangale ku kampani ya Salima Sugar.
Mneneri wa polisi mu dziko muno Peter Kalaya watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti ena amene awamanga ndi mkulu wakale wa bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority, (MERA) Collings Magalasi, mlembi wamkulu wakale ku office ya Pulezidenti Lloyd Muhara, mlembi ku nthambi yamsungichuma Cliff Chiunda ndi Jimmy Kusamale.
Pakadali pano anthuwa awatengera ku Polisi yaku Area 6 ku Lilongwe kumene akuyembekezera kuwatengera ku khothi kuti akawatsegulire mulandu.
Wolemba Phales Nthambo

Comments
Post a Comment