Bungwe la Malawi Bureau of Standards (MBS) lero laseka sitolo ya Sana Northern End ili kufupi ndi St Andrews CCAP komaso Sana Wholesale imene ili ku katoto muzinda wa Mzuzu.
Izi ndi malingana ndikusatsata ndondomeko za ukhondo musitolozi zomwe zaoneka pomwe bungweli limayendera sitolozi.
Mwazina sitolozi zatsekedwa kamba kopezeka ndi zakudya zoonongeka monga nyama, nsomba ndi zina komaso katundu oti masiku ake anatha (expire).
Bungwe la MBS lakhala likuyendera sitolo zosiyanasiyana ngat njira imodzi yoonesesa kuti ukhondo ukuyenda bwino.
Izi zikudza pomwe bungweli latsekanso sitolo za Sana ku Blantyre ndi ku Lilongwe pazifukwa zakusowa kwa ukhondo komanso kugulitsa zakudya zoonobgeka zomwe zimapereka chiopsezo chachikulu ku umoyo wa anthu mdziko muno mwa zina.
Wolemba Phales Nthambo


Comments
Post a Comment