Bwalo la milandu ku Blantyre latulutsa pa belo a Sameer Suleiman womwe Polisi ya Blantyre inawamanga lolemba atakazipereka wokha.
Asanamangidwe a Suleiman anamva kuti aPolisi akuwafuna pa Mulandu womwe malingana ndi aPolisi akuwaganizira kuti anafalitsa uthenga wabodza wokhudza anthu ena atatu.
Malingana ndi aPolisi woganiziridwawa adanena pa msonkhano wina wandale kuti Dr Ken Zikhale Ng'oma, Richard Chinwendo Banda komanso Baba Steve Malondela amachita upo wofuna kuwapha.
Lisanawatulutse bwalo la Blantyre magistrate linati a Suleiman akuyenera kupereka ndalama yokwana 500,000 kwacha komanso chikole Cha 2 million kwacha kuchokera kwa mboni ziwirizi.
Iwo awalamulanso kuti apereke zitupa zawo zoyendera komanso azikawonekera ku likuru la Polisi ku chigawo chakumwera kamodzi pa mwezi.
Olemba Phales Nthambo

Apa nde timati ndale zafikapo
ReplyDelete