Mtsogeleri wa Chipani Cha People's Development Kondwani Nankhumwa wauza khwimbi lomwe linasonkhana pa Sukulu ya Pulayimale ya Chindola m'boma la Mulanje kuti ndiyekhawo amene ali ndi kuthekera kodzathetsa mavuto akadzawavotera kukhala mtsogeleri wa dziko lino.
Iwo anenetsa kuti dziko lino likukumana ndi mavuto womwe akufunika utsogoleri watsopano ponena kuti utsogoleri wotere uli mwa iwo.
Asanapange chipani chawo a Nankhumwa anali wachiwiri kwa mtsogeleri wachipani chimene chinali m'boma Cha DPP ku chigawo chakumwera komanso anakhalapo nduna ya bomolo.
Wolemba Alice Moyo


Comments
Post a Comment