Mtsogoleri wachipani cha Democratic Proggresive Party (Dpp) Professor Ather Peter Muntharika akuchititsa misonkhano yoimayima mu mzinda wa Blantyre ndipo pano wafika kwachemusa.
Mwazina Muntharika watsindika kuti ndiokonzeka kulamulanso dziko lino ngati anthu angazamupatse voti pa chisankho Chapa 16 September 2025.
Muntharika akuti akazamusankha azathana ndi mavuto omwe anthu mdziko muno akukumana nawo pakadali pano.
Mtsogoleriyu walimbikitsanso anthu kuti akalembetse mu kaundula wachibwerenza cha kalembela wa chisankho yemwe akuyambiranso posachedwapa.
(Wolemba Alice Moyo)


Comments
Post a Comment